1 Chronicles 23:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Amuramu anali Aroni ndi Mose. Aaroni adampatula kuti aziyang'anira zinthu zopatulika za Mulungu. Iyeyo ndi ana ake ankapereka nsembe zofukiza pamaso pa Chauta mpaka muyaya, ndipo ankatumikira ndi kudalitsa anthu m'dzina la Chautayo mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Amiramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulikitsa, iye ndi ana ace, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kosatha.