1 Chronicles 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo amene anali ana a Levi potsata atsogoleri a mabanja a makolo ao, monga m'mene adalembedwera. Ankatsata chiŵerengero cha anthu kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo. Ameneŵa ndiwo amene ankayenera kugwira ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akuru a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa ciwerengo ca maina mmodzi mmodzi, akugwira nchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.