1 Chronicles 23:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ntchito yao idzakhala yothandiza ana a Aroni pa ntchito yaunsembe ya ku Nyumba ya Chauta. Azidzasamala mabwalo ndi zipinda, kuyeretsa zonse zimene zili zopatulika, ndiponso azidzagwira ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti nchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde nchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;