1 Chronicles 23:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali nayonso ntchito yosamalira buledi wopatulika, ufa wa nsembe yaufa, mitanda ya buledi wosatupitsa, nsembe zopereka m'chiwaya, nsembe yosanganiza ndi mafuta. Alinso ndi ntchito yoyesa ndi kupima nsembe zonse zoperekedwa m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda cotupitsa, ndi ya ciwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iri yonse;