1 Chronicles 23:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵerenga Aleviwo kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo. Chiŵerengero chao chinali anthu 38,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo ciwerengo cao kuwawerenga mmodzi mmodzi ndico amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.