1 Chronicles 23:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo azitero nthaŵi zonse akamapereka kwa Chauta nsembe zopsereza za masiku a Sabata, za pokhala mwezi uliwonse, ndiponso za pa chikondwerero china chilichonse chachipembedzo. Ntchito zotumikira Chautazi adzazichita kwamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwace monga mwa lemba lace, kosalekeza pamaso pa Yehova;