1 Chronicles 24:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ntchito yao ya anthu ameneŵa inali yotumikira m'Nyumba ya Mulungu potsata mwambo umene adaukhazikitsa Aroni kholo lao, monga momwe Chauta Mulungu wa Aisraele adaamlamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ciweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israyeli anamlamulira.