1 Chronicles 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zidzukulu za Aroni mfumu Davide adazigaŵira ntchito molongosoka bwino, pothandizidwa ndi Zadoki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleke wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.