1 Chronicles 24:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabanja ameneŵanso kuti adziŵe ntchito zao, adachita maere monga abale ao, zidzukulu za Aaroni, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Ochita umboni anali mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng'ono wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awanso anacita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akuru a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkuru wa nyumba za makolo monga mng'ono wace.