1 Chronicles 24:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti pakati pa zidzukulu za Eleazara padapezeka atsogoleri ambiri kupambana pakati pa zidzukulu za Itamara, Davide adasankhula atsogoleri 16 pakati pa zidzukulu za Eleazara, ndiponso asanu ndi atatu pakati pa zidzukulu za Itamara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapeza kuti amuna akulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapeza kuti amuna akuru a ana a Eleazara anacuruka, a ana a Itamara anacepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akuru a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.