1 Chronicles 24:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Magulu aŵiri a zidzukuluzi adachita maerewo motsatana, ndipo mlembi Semaya, mwana wa Netanele, amene anali Mlevi, adalemba maina ao. Mboni zake zinali izi: mfumu, nduna, wansembe Zadoki, Abimeleki mwana wa Abiyatara, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.