1 Chronicles 25:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide pamodzi ndi akuluakulu osamalira za utumiki adapatulanso anthu ena otumikira mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni amene ankalosa poimba ndi apangwe ndi azeze ndiponso ziwaya zamalipenga. Mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchitoyo ndiponso mndandanda wa ntchito zao nawu:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi ciwerengo ca anchito monga mwa kutumikira kwao ndko: