1 Chronicles 25:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali ana asanu ndi mmodzi a Yedutuni, maina ao naŵa: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Amene ankaŵatsogolera ndi bambo wao Yedutuni. Iwoŵa ankalalika ndiponso kuimba ndi pangwe pothokoza ndi kutamanda Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemeza Yehova ndi zeze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
A Yedntuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa cilangizo ca atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.