1 Chronicles 25:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo ankaimba potsata malangizo a bambo wao m'Nyumba ya Mulungu. Ankaimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira ku Nyumba ya Mulungu. Asafu, Yedutuni ndi Hemani inkaŵalamulira ndi mfumu imene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.