1 Chronicles 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onseŵa anali aluso pa zoimba, achibale ao nawonso adaaphunzira kwambiri kuimbira Chauta. Onse pamodzi analipo 288.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chiwerengo chao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.