1 Chronicles 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku banja la Merari kudasankhidwa Hosa amene anali ndi ana aŵa: Simiri mtsogoleri (iyeyu ngakhale sanali mwana wachisamba, atate ake adaamsankhula kuti akhale mtsogoleri.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkulu ndi Simiri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wake anamuyesa wamkulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkuru ndi Simri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wace anamuyesa wamkuru;