1 Chronicles 26:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alonda a pa khomo la Nyumba ya Chauta adaŵaika m'magulu, potsata mabanja ao, ndipo adaŵapatsa ntchito zao zotumikira, monga momwe adachitira Alevi anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akuchita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akucita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova.