1 Chronicles 26:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Selomoti pamodzi ndi abale ake, ndiwo amene ankasamalira mphatso zonse zopatulika zoperekedwa ndi mneneri Samuele, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndiponso ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndipo zinthu zina zonse zoperekedwa ndi munthu wina aliyense zinali m'manja mwa Selemoti ndi abale ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zonse adazipatula Samuele mlauli, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndi Yowabu mwana wa Zeruya; aliyense anapatula kanthu kalikonse, anazisunga Selomoti ndi abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zonse adazipatula Samueli mlauli, ndi Sauli mwana wa Kisi, ndi Abineri mwana wa Neri, ndi Yoabu mwana wa Zeruya; ali yense anapatula kanthu kali konse, anazisunga Selomoti ndi abale ace.