1 Chronicles 26:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa Ahebroni, Hasabiya pamodzi ndi abale ake 1,700, anthu anzeru, ankayang'anira Aisraele chakuzambwe kwa Yordani, pa ntchito zonse za chipembedzo ndiponso za boma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake odziwa mphamvu chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israele tsidya lino la Yordani kumadzulo, kuyang'anira ntchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ace odziwa mphamvu cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israyeli tsidya lino la Yordano kumadzulo, kuyang'anira nchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.