1 Chronicles 26:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeriya ndiye anali mtsogoleri wa Ahebroni potsata mndandanda wa mabanja a makolo. Pa chaka cha 40 cha ufumu wa Davide padachitika kafukufuku ndipo padapezeka kuti ena otchuka a m'banja la Yeriya ankakhala ku Yazere ku Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yeriya ndiye mkulu wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Chaka cha makumi anai cha ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazere wa ku Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yeriya ndiye mkuru wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Caka ca makumi anai ca ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazeri wa ku Gileadi.