1 Chronicles 26:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Davide adasankha atsogoleri okwanira 2,700 a m'banja la Yeriyayo kuti aziyang'anira Arubeni, Agadi ndiponso fuko lahafu la Amanase pa zonse zokhudza chipembedzo ndiponso za boma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi abale ake ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akulu a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi abale ace ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akuru a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.