1 Chronicles 26:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku banja la Obededomu kudasankhidwa anthu 62, onsewo okhoza ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onsewa ndiwo a ana a Obededomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obededomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onsewa ndiwo a ana a Obedi Edomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obedi Edomu.