1 Chronicles 27:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu mndandanda wa atsogoleri a mabanja a Aisraele olamulira ankhondo zikwi ndiponso ankhondo mazana, pamodzi ndi akulu ao amene ankatumikira mfumu. Ankasinthanasinthana mwezi ndi mwezi pa chaka chilichonse, gulu lililonse linali ndi anthu okwanira 24,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli monga mwa ciwerengo cao, kunena za akuru a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu nchito iri yonse ya magawidwe, akulowa ndi kuturuka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya caka, cigawo ciri conse nca amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.