1 Chronicles 27:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu mwana wa Zeruya adayambapo kuŵerenga, koma sadatsirize ai. Mkwiyo wa Chauta udaŵagwera Aisraele chifukwa cha zimenezi, ndipo chiŵerengerocho sadachiloŵetse m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.