1 Chronicles 27:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azimaveti mwana wa Adiyele ankayang'anira chuma cha mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayang'anira chuma cham'miraga, cham'mizinda, cham'midzi ndi cha m'nyumba zankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo woyang'anira chuma cha mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyele, ndi woyang'anira wa chuma cha m'minda, m'mizinda ndi m'milaga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;