1 Chronicles 27:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yonatani, mtsibweni wake wa Davide, anali phungu wake, popeza kuti anali munthu womvetsa zinthu, ndiponso wophunzira bwino. Iyeyo pamodzi ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni, ankaphunzitsa ana a mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yonatani atate wace wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehieli mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;