1 Chronicles 27:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahitofele atamwalira, m'malo mwake mudaloŵa Yehoyada, mwana wa Benaya, ndiponso Abiyatara. Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara. Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi wotsatana ndi Ahitofeli, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yoabu.