1 Chronicles 28:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adasonkhanitsa ku Yerusalemu akuluakulu onse a Aisraele, ndiye kuti akuluakulu a mafuko, akapitao a magulu amene ankatumikira mfumu, atsogoleri a ankhondo zikwi, atsogoleri a ankhondo mazana, akulu osunga katundu yense ndi ng'ombe za mfumu ndi za ana ake, pamodzi ndi akulu oyang'anira nyumba ya mfumu, anthu amphamvu, ndiponso ngwazi zonse zankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga Israyeli, a akalonga a mapfuko, ndi akuru a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akuru a mazana, ndi akuru a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ace; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.