1 Chronicles 28:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono uganizire bwino zimenezi, pakuti Chauta wakusankha iweyo kuti ummangire nyumba, m'mene Iye azikhalamo ngati mwake. Limba mtima tsono, ndipo uigwire ntchitoyi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nucite.