1 Chronicles 28:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaperekanso pulani ya zonse zimene ankaziganizira za mabwalo a Nyumba ya Chauta, ya zipinda zonse zozungulira, ya nyumba zosungiramo chuma cha m'Nyumba ya Chauta, ndiponso ya nyumba yosungiramo mphatso zopatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chifaniziro cha zonse anali nazo mwa mzimu, cha mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi cha zipinda zonse pozungulirapo, cha zosungiramo chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi cha zosungiramo chuma za zinthu zopatulika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi cifaniziro ca zonse anali nazo mwa mzimu, ca mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi ca zipinda zonse pozungulirapo, ca zosungiramo cuma za nyumba ya Mulungu, ndi ca zosungiramo cuma za zinthu zopatulika;