1 Chronicles 28:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adafotokoza za magaŵidwe a magulu a ansembe ndi a Alevi, ndiponso magaŵidwe a ntchito zonse za m'Nyumba ya Chauta. Adafotokozanso za ziŵiya zonse zogwira nazo ntchito m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi cha magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi cha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi cha zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ca magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi ca nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi ca zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;