1 Chronicles 28:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kulemera kwa golide wa zoikapo nyale pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa golide wa choikaponyale chilichonse chagolide pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa siliva wa choikaponyale chasiliva pamodzi ndi nyale zake, potsata ntchito ya choikaponyale chilichonse,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwa kulemera kwakenso cha zoikapo nyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikapo nyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikapo nyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikapo nyali chilichonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwa kulemera kwacenso ca zoikapo nyali zagolidi, ndi nyali zace zagolidi, mwa kulemera kwace ca coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace; ndi ca zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwace wa coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace, monga mwa coikapo nyali ciri conse;