1 Chronicles 28:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalangiza za kulemera kwa golide wopangira guwa la zofukiza, ndiponso pulani ya guwalo. Adapereka pulani ya galeta lagolide, ndiye kuti akerubi amene ankatambasula mapiko ao kuphimbira Bokosi lachipangano la Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta wa akerubi agolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ca guwa la nsembe lofukizapo la golidi woyengetsa woyesedwa kulemera kwace, ndi cifaniziro ca gareta wa akerubi agolidi akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la cipangano la Yehova.