1 Chronicles 28:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Davide adaimirira nati, “Tamverani abale anga ndiponso anthu anga. Ine ndinkaganiza zomanga nyumba yokhalamo Bokosi lachipangano la Chauta, limene lili ngati malo opondapo mapazi Mulungu wathu. Ndipo ndidakonza zomangira nyumbayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Davide anaima ciriri, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la cipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.