1 Chronicles 28:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Magulu a ansembe ndi a Alevi oyenera kugwira ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta ngokonzeka ndithu. Ndipo iwe, pa ntchito yonseyo, udzakhala nawo anthu aluso odzipereka pa ntchito yao. Anthu wamba onse ndi atsogoleri ao omwe uzidzaŵalamulira ndiwe zoti achite.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu ntchito iliyonse pali onse ofuna eni ake aluso, achite za utumiki uliwonse; akulu omwe ndi anthu onse adzachita monga umo udzanenamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu nchito iri yonse pali onse ofuna eni ace aluso, acite za utumiki uli wonse; akuru omwe ndi anthu onse adzacita monga umo udzanenamo.