1 Chronicles 28:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Chauta, Mulungu wa Israele, adandisankha ine pakati pa onse a m'banja la kholo langa, kuti ndikhale mfumu ya Israele mpaka muyaya. Pajatu Iyeyo adasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri wa mafuko onse, ndipo ku fuko la Yuda adasankhako banja la bambo wanga. Ndipo pakati pa ana a atate angawo kudakomera Mulungu kuti asankhe ine, kuti ndikhale mfumu ya Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Komatu Yehova Mulungu wa Israele anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israele kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israele yense;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komatu Yehova Mulungu wa Israyeli anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israyeli kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israyeli yense;