1 Chronicles 28:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ufumu wake ndidzaukhazikitsa mpaka muyaya, akalimbikiradi kumvera malamulo ndi malangizo anga, monga momwe akuchitira tsopano.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kosatha, akalimbika kuchita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace kosatha, akalimbika kucita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.