1 Chronicles 28:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono pamaso pa Aisraele onse ndiponso pamaso pa msonkhano umenewu, Mulungu wathu alikumva, ndikukuuzitsani kuti muzisunga ndi kusamala malamulo onse a Chauta Mulungu wanu, kuti mukhalitse m'dziko labwinoli, ndipo lidzakhale nthaŵi zonse choloŵa cha ana anu, inu mutapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, pamaso pa Aisrayeli onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanu lanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu colowa cao kosalekeza.