1 Chronicles 28:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, uzimvera Mulungu wa atate ako, ndipo uzimtumikira ndi mtima wonse, modzipereka kwathunthu. Paja Chauta amasanthula mtima wa munthu aliyense, ndipo amadziŵa maganizo a munthu aliyense. Ukamfunafuna, udzampeza. Koma ukalekana naye, Iyeyo adzakutaya mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.