1 Chronicles 29:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Solomoni mwana wangayu, amene Mulungu yekha wamsankha, akali wamng'ono ndi wosadziŵa zambiri, ndipo ntchitoyi njaikulu. Nyumbayi sidzakhala ya munthu koma ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomo yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo nchitoyi ndi yaikuru, pakuti cinyumbaci siciri ca munthu, koma ca Yehova Mulungu.