1 Chronicles 29:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo mucita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikuru; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.