1 Chronicles 29:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, Mulungu wa makolo athu aja, Abrahamu, Isaki ndi Israele, limbitsani nthaŵi zonse maganizo ndi makhalidwe ameneŵa mwa anthu anu, ndipo akhale ndi mtima wokhulupirika mpaka kwa Inu muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isaki, ndi wa Israele makolo athu, musungitse ichi kosatha m'chilingaliro cha maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isake, ndi wa Israyeli makolo athu, musungitse ici kosatha m'cilingaliro ca maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,