1 Chronicles 29:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wanga Solomoni mumpatse mtima wangwiro, kuti azisunga malamulo ndi malangizo anu ndi kuŵatsata bwino ndithu, ndiponso kuti amange nyumba imene ine ndaipezera zofunika zonsezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nimupatse Solomo mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kucita izi zonse, ndi kumanga cinyumbaci cimene ndakonzeratu mirimo yace,