1 Chronicles 29:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidapereka za ku Nyumba ya Chauta wanga monga m'mene ndidathera, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuŵa wopangira zinthu zamkuŵa, chitsulo chopangira zinthu zazitsulo ndi mitengo yopangira zinthu zamtengo. Ndidaperekanso miyala yochuluka yomangira, ya mtundu wa onikisi, miyala ya maŵangamaŵanga, miyala yambiri yamitundumitundu yamtengowapatali ndiponso miyala ya marabulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golidi wa zija zagolidi ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, citsulo ca zija zacitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawanga mawanga, ndi miyala ya mtengo wace ya mitundu mitundu ndi miyala yansangalabwe yocuruka.