1 Chronicles 29:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwace mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe cikwi cimodzi, nkhosa zamphongo cikwi cimodzi, ndi ana a nkhosa cikwi cimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zocuruka za Aisrayeli onse: