1 Chronicles 29:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri. Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi cimwemwe cacikuru. Ndipo analonga ufumu Solomo mwana wa Davide kaciwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.