1 Chronicles 29:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anakuza Solomo kwakukuru pamaso pa Aisrayeli onse, nampatsa ulemerero wacifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israyeli inali nao wotero.