1 Chronicles 29:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israyeli ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.