1 Chronicles 29:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, cuma cangacanga ca golidi ndi siliva ndiri naco ndicipereka ku nyumba ya Mulungu wanga, moenjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;