1 Chronicles 29:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
golide wa zija zagolide, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za ntchito zilizonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero lino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
golidi wa zija zagolidi, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za nchito ziri zonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero line?